MSAKAKUONA, AKIDU NDI MPONDA ALIMBIRANA MPHOTO YA MPHUNZITSI WAPAMWAMBA
Aphunzitsi a Blue Eagles De Kleck Msakakuona, yemwe anali wogwirizira ku Ekhaya Fundi Akidu komanso wa Masters FC Peter Mponda alimbirana pa mphoto ya mphunzitsi wapamwamba mu mwezi wa May mu FDH Premiership.
Mayinawa atulutsidwa ndi bungwe la Super League of Malawi lachinayi pomwe mphotozi zikuyamba tsopano kuperekedwa.
Msakakuona anatsogolera Blue Eagles ku zipambano zinayi, kufananitsa mphamvu kamodzi ndi kugonjanso kamodzi pa masewero asanu ndi amodzi oyambilira mu ligiyi kuthandizira kuti timuyi ikhale kumtunda kwa ligiyi.
Akidu, yemwe anagwirizira ntchitoyi kutsatira kutenga tchuthi kwa Enos Chatama, anakwanitsa kutsogolera zipambano zitatu ndi kugonja kamodzi pa masewero anayi pansi pa iye.
Ndipo Mponda anakwanitsa kutsogolera timuyi ku zipambano zinayi ndi kugonja kawiri mu Chaka choyamba cha timuyi pa masewero asanu ndi amodzi.
Yemwe atenge mavoti ochuluka pa atatuwa ndi yemwe atalandire mphotoyi ku
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores