"TIMU TSOPANO IKUBWERAMO" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya LUANAR Mitundu Oscar Kaunda wati tsopano osewera ake akubweramo pomwe akukwanitsa kumva zomwe iye akuwauza ndipo zatsala zinthu zochepa kuti timuyi ikhazikike.
Iye amayankhula atatha kugonjetsa Blue Eagles 3-2 pa bwalo la Dedza loweruka pomwe Vincent Nyangulu anamwetsa chigoli chimodzi ndipo Raheem Mtondera anagoletsa ziwiri koma Farhad Mtcheka ndi Micium Mhone anabwenzako mu nthawi yoonjezera.
Kaunda anayamikira osewerawa kamba kosewera bwino komanso koyesetsa kuti azitolera mapoints mu masewero apakhomo mu ligiyi.
"Sabata yatha tinagonja ku mpoto koma tinawauza kuti sitikufunika kugonjanso kawiri nde zatheka lero, timu ikubweramo tsopano pomwe akumamva zomwe tikuwauza," anatero Kaunda.
Iye koma wati chatsala choti akwanitse kupeza chipambano koyenda ndipo zikatero ndekuti chilichonse chikhala Kuti chilibwino kwambiri.
Timuyi tsopano ili ndi mapoints okwana 10 mu ligi pomwe ili pa nambala 9 itapambana katatu, kufanana mpha
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores