ZASINTHANSO
Bungwe loyendetsa ligi yaikulu ya mdziko muno la Super League of Malawi lalengeza kuti masewero a FCB Nyasa Big Bullets komanso Masters FC adzaseweredwa lolemba pa bwalo la Mpira mu mzinda wa Blantyre.
Masewero anasinthidwa kuchoka bwalo la Mpira kupita ku bwalo la Joyce Chitsulo ku Mwanza loweruka koma patsikuli mabwalo onsewa adzakhala otanganidwa.
Zateremu, Bullets ikuyembekezeka kusewera masewero awo oyamba apakhomo pa bwalo la Mpira monga mwa kukhumba kwawo kamba koti ku Mwanza timuyi ikumavutikako.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores