"ANATIYANKHULA MU CHINGEREZI NDIPO TINAMVA" - MPOKERA
Mtsogoleri wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Blessings Mpokera, wati palibe chophinja chilichonse chomwe apeze pa kuyankhulana ndi mphunzitsi watsopano wawo, Wedson Nyirenda, kamba koti chizungu chili paliponse.
Iye amayankhula pofotokozapo momwe osewerawa amulandilira mphunzitsiyu yemwe walembedwa ntchito kutimuyi lachitatu ndipo kwawo ndiku Zambia.
Mpokera anati mphunzitsiyu anawayankhula lachinayi atafika ku zokonzekera zawo ndipo atha kukhala mlendo ku timuyi koma si mlendo ku mpira.
"Zomwe anatiuza ndi zomwezo zimene aphunzitsi ena onse akhala akutiyankhula nde sitinamulandire, timulandira loweruka tikapambana," anatero Mpokera.
Iye anati chingerezi ndi chiyankhulo chabe chomwe angakhale mmayiko a aluya chimapezeka kamba koti ndi chomwe anthu osiyanasiyana amamvana ndipo Nyirenda akugwiritsa ntchitodi chizungu koma akukwanitsa kumva.
Patsogolo pokumana ndi Ekhaya, iye wati osewera onse akonzeka kuti achite bwino
ndikumulandira mphunzitsiyu.
Bullets ikumana ndi Ekhaya mu ndime ya matimu asanu ndi atatu mu chikho cha Airtel Top 8 pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe loweruka madzulo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores