CIVIL IKUFUNITSITSA KUCHITA BWINO KOYENDA
Mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Abbas Makawa, wati timu yake ikufunitsitsa kuti igoletse zigoli zodutsa ziwiri pa masewero awo oyamba mu chikho cha Airtel Top 8 kuti asadzavutike mu masewero awo achibwereza pakhomo.
Makawa amayankhula patsogolo pa masewero omwe akumane ndi Blue Eagles mu ndime ya matimu asanu ndi atatu pa masewero oyamba pa bwalo la Bingu mu mzinda.
Iye wati akudziwa kuti timu yake ikuvutika mu ligi pomwe agonja masewero atatu otsogozana koma masewero amu chikho amakhala osiyana kwambiri ndipo akuyembekeza kuti achite bwino.
"Tikufunitsitsa kuti tigoletse zigoli ziwiri kapena zambiri kamba koti tili koyenda ndiye kuti pakhomo zitha kudzatiphwekera. Ndi zosiyana kuti Blue Eagles imangosewera masewero pa bwalo la Civo pomwe ifeyo timayambira pokonzekera nde sizoopsa mmasewero achibwerenzawo," anatero Makawa.
Ndipo mtsogoleri wa wosewera kutimuyi, Righteous Banda, wati akuyembekezera kukhala ndi masewero ovuta
kamba koti amavutitsana ndi Blue Eagles.
"Masewero awawa tikufuna akhale oti titembenuze zinthu kamba koti tagonja kwambiri nde ine ndi anyamata anga takonzeka kwambiri," anatero Banda.
Timu ya Civil inakwanitsa kuzigulira malo mu mpikisanowu itamaliza pa nambala yachisanu mu ligi ya chaka chatha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores