"IMENE IJA SINALI PENATE" - JOMO
Mphunzitsi wamkulu watimu ya Bangwe All Stars wapempha oyimbira kuti azipanga ziganizo zolondola pa masewero omwe aziyimbira ponena kuti ziganizo zolakwika zimapweteketsa matimu.
Iye amayankhula poonetsa kusakhutira ndi ntchito ya oyimbira pa masewero omwe alepherana 1-1 ndi FOMO FC pa bwalo la Mpira mu NBS Bank National Division League.
Osman wati penate yomwe FOMO inapatsidwa kuti ipeze chigoli chobwenzera mmasewerowa inali yabodza kupangitsa timu yawo kusachita bwino.
"Penanso oyimbirawa azipanga ziganizo zabwino chifukwa goloboyi wagwira mpira koma wosewera wa FOMO kukangoziponyapo basi ayimba. Mumajambula mukaonenso ngati ilidi penate," anatero Jomo.
Iye anatinso timu yake ikungodutsa mu nyengo yoipa kamba koti ikukanika kupeza chipambano koma ikusewera bwino ndipo posachedwapa ayamba kuchita bwino.
Bangwe yakhalabe pa nambala yachikhumi mu ligi pomwe ili ndi mapoints awiri itafananitsa mphamvu kawiri ndi kugonja kawirinso.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores