Haiya akukhulupilira kuti boma likonza ma bwalo
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, wati ali ndi chikhulupiliro kuti boma likhale likukonza ma bwalo osiyanasiyana mdziko muno kamba koti ndi boma lakumva ndipo awamvera mapempho awo.
Iye amayankhula pomwe anali mu boma la Thyolo pa masewero omwe Nchema United inalepherana 0-0 ndi Mighty Wanderers Reserve pa masewero amu FINCA Southern Region Division League One lamulungu masana pa bwalo la Nchima.
Iye anati bwalo la Thyolo lomwe likadamangidwabe komanso ma bwalo a Kamuzu ndi Mzuzu pambali pa ena ali mmanja mwa boma ndipo akukhulupilira kuti ntchito zomwe zikugwilidwa pa mabwalowa zikhale zikutha posachedwa.
"Mpira umatilumikizitsa posatengera kusiyana mtundu, khungu kaya chipani, nde takhala tikupempha boma kuti atimalizire bwalo la Thyolo poti lili mmanja mwawo nde poti ndi boma lokumva za anthu, ndikukhulupilira kuti atikonzera pamodzi ndi mabwalo ena ngati Kamuzu ndi Mzuzu mu masiku akudzawa,"
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores