FAZILI WATHOKOZA FAM PA MASEWERO AUBALE
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, wayamikira bungwe la Football Association of Malawi popereka mwayi kutimuyi wokhala ndi masewero apaubale patsogolo pa mpikisano wa Women's African Cup of Nations womwe wuseweredwe mu July chaka chino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe akukumana ndi timu ya Tanzania lachitatu masana m'dziko la Tanzania lomweli.
Fazili wati timuyi ili ndi osewera ambiri omwe akhala akuyenda nawo mu masewero ammbuyomu ndipo kusapezeka kwa osewera ena sikungawadandaulitse kamba koti omwe alipowo agwira ntchito.
Iye watinso masewerowa amupatsa mpata wabwino woona momwe timuyi ilili patsogolo pa mpikisano wa WAFCON.
"Zindipatsa mpata kuti ndione malo omwe tikuyenera kukonzabe komanso malo omwe tikuchita bwino nde masewerowa atichitira ubwino," anatero Fazili.
Iye wati kutenga osewera a timu ya atsikana osadutsa zaka 20 ngati Victoria Mkwala komanso Fatima Lali ndi kuwakonzekeretsa kuti ena akamakula iwo a
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores