"TIKUPEREKA OSEWERA KU MATIMU AKULUAKULU" - MAKONYOLA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Audlow Makonyola, wati kupeza mapoints asanu pa maseweronso asanu kwa timuyi sikuti ndi zoipa kutengera kuti osewera ake ambiri ndi achisodzera ndipo sanayizolowere ligi yaikulu.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-1 ndi timu ya Mighty Wanderers pa bwalo la Mpira ku Blantyre lachitatu masana.
Iye wati timu yake inayamba motsika kwambiri ndi chifukwa chake inangopereka zigoli kupangitsa kuti agonje.
"Osewera 6 omwe anali mu timu ija akuchokera Ku timu yaing'ono kusonyeza kuti timuyi ndi yatsopano nde zitengabe ka nthawi kuti igwirane bwinobwino koma zikhala bwino," anatero Makonyola.
Iye wati timu yake ikupereka chilimbikitso kuti ikhala yapamwamba kamba koti inaonetsa mpira wokongola ngakhale kuti agonja ndi zigoli zochuluka.
Timuyi ikhalabe pa nambala 12 mu ligi angakhale yagonja poti ikadali ndi mapoints asanu pa masewero asanu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores