KARONGA YAKONZEKA KUKUMANA NDI WANDERERS
Timu ya Karonga United yati ilibe mantha aliwonse patsogolo pa masewero awo ndi Mighty Wanderers ponena kuti akonzekera bwino masewerowa.
Mphunzitsi watimuyi, Audlow Makonyola, wayankhula mawuwa patsogolo pa masewerowa lachitatu pa bwalo la Mpira ndipo wati angakhale kuti anyamata atopa koma akasewerabe mmasewerowa.
"Anyamata akuoneka bwinobwino, sanatsikiretu poti tinali ndi masewero pompano. Kupambana ndi Civil ndi chilimbikitso chachikulu patsogolo pa masewerowa nde tikayesetsabe kuti tikatole kenakake," anatero Makonyola.
Iye watinso timu yake ilibe wosewera aliyense yemwe ndi wovulala ndipo chilichonse chili mchimake patsogolo pa masewerowa.
Timuyi ikulowa mmasewerowa ili pa nambala 9 pomwe ili ndi mapoints asanu pa masewero anayi omwe asewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores