GADDIE, SILWIMBA APEZEKA NDI KARONGA
Timu ya Mighty Wanderers yatsimikiza kuti akatswiri awo, Gaddie Chirwa ndi Timothy Silwimba, apezeka pa masewero omwe akukumana ndi Karonga United lachitatu pa bwalo la Mpira.
Mphunzitsi watimuyi, Bob Mpinganjira, ndi yemwe watsimikiza za nkhaniyi pofotokoza momwe timuyi yakonzekerera patsogolo pa masewerowa.
Chirwa anali pa chilango kamba koti analandira kadi yofiyira pomwe ankakumana ndi FCB Nyasa Big Bullets pomwe Silwimba wakhala ali wovulala kuchokera chaka chatha ndipo onsewa atha kupezeka mmasewerowa.
Mpinganjira wati masewerowa ndi ofunikira kwambiri kuti apambane kamba koti akusewerera pakhomo pawo.
"Sitikufuna kupereka phuma Kwa osewera ndi ife aphunzitsi ayi koma tikasewera masewero athu ndi mtima woti tikapambana zitikhalira bwino nde tikayesetsa kuti zikatiyendere," anatero Mpinganjira.
Iye wati ndi wokhutira ndi momwenso osewera omwe agulidwa kumene achitira ndipo akuyembekeza Zambiri Kwa Iwo.
Manoma alowa mmasewerowa ali pa nam