Katswiri wosewera pakati komanso kumbuyo kwa Mighty Wanderers, Dalitso Nahipa, wasankhidwa kuti ndi yemwe wasewera mwapamwamba mu sabata yachinayi yamasewero kutimuyi.
Iye wapambana mphotoyi atapeza mavoti ochuluka pamwamba pa Dan Kudonto komanso Dalitso Khungwa.
Iye walandira ndalama zokwana K300,000 kuchokera ku kampani ya Kingbossi yomwe ikupereka thandizo ku timuyi.
Nahipa anapatsidwa mwayi woyamba masewero kutimuyi koyamba pomwe anakumana ndi Silver Strikers ndipo anasewera mwapamwamba pa masewerowa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores