"BULLETS SIMAOPA TIMU ILIYONSE" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Gilbert Chirwa, wati timu yake ilibe mantha kukumana ndi Blue Eagles yomwe inawavutitsa Chaka chatha ponena kuti palibe timu yomwe timu yawo imayiopa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe akumane loweruka pa bwalo la Civo ndipo wati ndi yokonzeka kusewera masewerowa.
Chirwa anati akudziwa bwino kuti osewera ake anavutika mu masewero apitawo koma aunikira zomwe zinawavuta cholinga achite bwino.
"Ku Bullets kumakhaladi phuma nthawi zonse, tikakhala kuti tagonja nde lambiri koma limachepako tikapambana. Ifeyo sitimaopa timu iliyonse, nthawi zina timatha osachita bwino koma nthawi zambiri ndi ifeyo timachita bwino," anatero Chirwa.
Iye anatinso kusapezeka kwa Sean Mcbrams ndi chifukwa choti anachokapo nthawi ya zokonzekera kupita ku South Africa ndipo sanazikokere minyewa.
Timuyi ikulowa mu masewero awo achisanu ili ndi mapoints okwana asanu ndi atatu kutsatira kuti apambana kawiri ndi kufana
mmmmmmmmm
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores