KARONGA IKUFUNA K26 MILLION KAPENA SAPITA KU BLANTYRE
Timu ya Karonga United yati ikufuna ndalama zokwana K26 million zomwe anaononga pokonzekera masewero omwe analephereka pa tsiku lotsegulira ligi ya chaka chino ngati bungwe la Super League of Malawi likufuna kuti akasewere ndi Mighty Wanderers lachitatu.
Timuyi yayankhula izi kutsatira kuikidwa kwa masewerowa kuti akaseweredwa pa bwalo la Mpira lachitatu pofuna kukwanilitsa masewero omwe analepherekawa.
Poyankhula ndi wayilesi ya Zodiak, mlembi wa timuyi, Romzy Simwaka, wati timu yake siyipitako ku Blantyre ngati sapatsidwa ndalamazi.
"Anatiuza a SULOM kuti masewero aja atha kuseweredwa mkati mwa sabata zimene tinavomera koma tinawauza kuti atibwenzere ndalama zomwe tinaononga pa ulendo woyamba nawonso anavomera nde tikungodikira. Ngati silowa ndekuti tithera mu Lilongwe," anatero Simwaka.
Iye anatinso ngati akuwerengera ndalama yapa zipata yomwe timuyi inapatsidwa pa masewero olepherekawa, a SULOM atha kuchotserapo ndalamayi n
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores