SULOM YANGOTSITSA MTENGO
Bungwe la Super League of Malawi lalengeza kuti masewero a timu ya Mighty Wanderers komanso Karonga United atsitsidwa mtengo.
Izi zikutsatira kuti ochemerera anaperekanso ndalama pa masewero omwe analephereka mwezi watha pa tsiku lotsegulira ligi ya FDH Premiership.
Kamba ka kuvuta kuti adzazindikire omwe analowa mu masewerowa poyamba, bungweli langopanga chiganizo kuti lingotsitsa mtengo kuchoka pa K7,000 kufika pa K4,000.
Masewerowa adzaseweredwa pa bwalo la Mpira pofuna kusokerera masewero omwe analepherekawa komanso ganizo lomwe anthu amati adzalowa ulere silichitika.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores