CRECK YAIMITSA AUPHUNZITSI AKE
Timu ya Creck Sporting Club yalengeza kuti yaimitsa ntchito kaye mphunzitsi wamkulu, Eliya kananji komanso wachiwiri wake Harry Saidi kamba ka kusachita bwino Kwa timuyi.
Malingana ndi uthenga womwe timuyi yatsimikiza pa tsamba lawo la mchezo madzulo a lamulungu, kuyimitsidwaku ndi kwa pompompo ndipo akhale akufotokoza chitsogolo cha nkhaniyi.
Timuyi yayamba movutika kwambiri pomwe yagonja masewero onse apakhomo ndi kufananitsa mphamvu onse akoyenda kuti akhale ndi mapoints awiri okha mu ligi.
Iwo agonja ndi Mighty Wanderers 2-1 komanso Kamuzu Barracks 3-1 komanso kufananitsa mphamvu ma 1-1 ndi Red Lions komanso MAFCO koyenda mu ligi.
Kananji anapita kutimuyi kuyisiya timu ya Blue Eagles yomwe anatuluka nayo ndi kuyilowetsanso mu ligi yaikulu ya mdziko muno.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores