"NGATI MPIRA KU MALAWI UKUONONGEKA NDI OYIMBIRA" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Abbas Makawa, wati oyimbira a mdziko muno akuononga mpira kwambiri ndi kayimbilidwe koipa kopondereza matimu ena ndipo akanakhala kuti amasewera kwawo akanatha kupambana 5-0 ndi Chitipa United.
Iye amayankhula atatha masewero omwe timu yake yagonja 1-0 ndi timu ya Chitipa United pa bwalo la Chitipa kukhala masewero oyamba kuti agonje chaka chino ndipo wadandaula kwambiri ndi oyimbira.
Iye wati ngati matimu ena ali abwino azikwanitsanso kupambana koyenda osati pakhomo pokha chifukwa choti amathandizidwa ndi oyimbira.
"Atichinyadi chigoli chabwinobwino chopanda vuto inde koma kayimbilidwe kake koseketsa kwambiri. Tinapeza chigoli chabwinobwino koma anachikana amadziwa kuti tikatsogola akanika kubweramo akunowa, Ife tasewera bwino palibe chovuta koma kuyimbiraku ndi komwe katipweteka," iye anatero.
Iye wapempha kuti oyimbirawa kuti akhale opanda mbali zomwe zithandizire kumapereka chi
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores