KULIBE MOWA NDI YAMALOVA KU DERBY
Bungwe loyendetsa ligi yaikulu ya m'dziko muno la Super League of Malawi lalengeza kuti mabotolo a galasi, mowa komanso malova zonse sizikaloledwa pa masewero omwe Mighty Wanderers ikumane ndi FCB Nyasa Big Bullets lamulungu pa bwalo la Bingu.
Malingana ndi uthenga womwe bungweli lapereka lachisanu mmawa, iwo ati mabotolo a galasi ndi mowa sizikaloledwa mkati mwa bwalo komanso poyandikira bwaloli kamba koti anthu amasandutsa kukhala zogenderana ndi kuvulazana.
Iwo atinso nthawi ya malova yomwe imaperekedwa mphindi 15 zakumapeto zomwe anthu omwe alibiretu ndalama amalowa mubwalo sikaperekedwa ndipo akangotsegula wayilesi ndi kukhala kwawo.
Masewerowa adzayamba nthawi ya hafu pasiti 4 ndipo timu ya Mighty Wanderers ndi yomwe ili pakhomo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores