Kampani ya World Star Betting yaonjezera mgwirizano wake ndi timu ya Blue Eagles pomwe iziyika ndalama zokwana K100 million mu ligi ya chaka chino.
Kampaniyi yapereka yunifolomu yapamwamba kutimuyi ndipo ndalamayi igwira ntchito popereka wosewera wapamwamba pa masewero aliwonse ndi ndalama yokwana K150,000 komanso ndalama yopereka kwa osewera akatha masewero komanso ndalama zosainira mgwirizano za osewera.
Mwambo wosayinirana mgwirizanowu unachitika lachitatu ku ma ofesi a likulu la polisi ku Area 30 mu mzinda wa Lilongwe.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores