Banki ya National yakhutira ndi ligi zomwe amathandiza
Banki ya National yati ndi yokondwa ndi momwe mpikisano yomwe amathandiza ya NBM Women's Premiership komanso NBM U-23 Football Championship ayendera poti kunalibe ziwawa zilizonse mmabwalo.
Izi zayankhulidwa pa mwambo wumene bankiyi imapereka mphoto kwa atolankhani omwe anasankhidwa kuti alemba mwapamwamba nkhani zokhudza mipikisano iwiriyi mu chaka cha 2025-26.
Mmodzi mwa akuluakulu a bankiyi, Oswin Kasunda, wati ndi wokondwa khumbo lawo lomwe amafuna kuti atukule mpira kuchokera pansi ndi kumudzi zakwanilitsa mu chaka chomwe anayika thandizo lawo.
"Takhala tikutsatira mmene mipikisanoyi imayendera ndipo tapeza kuti yatulutsa luso lochuluka kwambiri nde ifeyo ndife okhutira chifukwa zayenda bwino, sitinamveko ziwawa moti dzina lathu lapita patsogolo kwambiri," anatero Kasunda.
Ndipo mtsogoleri wa FAM Fleetwood Haiya wati mpikisanowu wayendetsedwa mwa ukadaulo zomwe zithandizira kuti luso la osewera lipite patsogolo.
"Tili ndi chikhulupiliro kuti momwe tayendetsera mipikisanoyi a banki ya National akhalabe nafe. Ndimanena kuti FAM yapanoyi si yoti ingamasowe othandiza ayi chifukwa muli chilungamo mu kayendetsedwe kake kamba koti timayika za Ife pamtunda Kuti anthu awone," anatero Haiya.
Iye anatinso kupezeka kwa Deborah Henry kuonedwa kuti apite ku Scorchers komwenso akuchita bwino, kugulidwa kwa Sarah Mlimbika ndi timu yaku Zambia komanso osewera a zaka zosadutsa 23 kupita ku matimu akuluakulu ngati Silver Strikers ndi zina mwa zomwe adzakumbukire kuti akwanilitsa kudzera mu mipikisanoyi.
Bankiyi inayika ndalama zokwana K1.5 billion pa mipikisanoyi yomwe wa amayi ndi woyamba kukhala wa dziko lonse ngati ligi ndipo winayo unali woseweredwa mu ma boma onse amu dziko muno.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores