"MASEWERO A ACHINA WANDERERS AMAKHALA OPHWEKA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Eliya Kananji, wati kukumana ndi matimu omwe amadziwika kuti ndi akuluakulu kumakhala kophweka kuti apambane ndipo Mighty Wanderers iziona ku Mchinji.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko pa bwalo la Aubrey Dimba lamulungu ndipo wati iwo akufunitsitsa kupambana mmasewerowa.
"Amakhala masewero ophweka kusiyana ndi matimu omwe amaoneka ngati ang'onoang'ono aja nde awa akutipeza pakhomo tikayesetsa kuti tikawachinye ndithu," iye anatero.
Timuyi sikhala ndi goloboyi Donnex Mwakasinga ndi Auspicious Kadzongola omwe ndi ovulala koma Kananji wati osewera ena aliponso.
Creck Sporting Club siyinagonjetseko Wanderers chiyambireni ndipo ili ndi point imodzi pa masewero amodzi omwe analepherana 1-1 ndi Red Lions sabata yatha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores