CIVIL YAGONJA KATATU KOTSATIZANA MU LIGI
Timu ya Civil Service United yagonja katatu kotsogozana mu ligi ya FDH Premiership kusiyana ndi momwe anayambira mu masewero awo atatu oyamba pomwe agonja 3-0 ndi LUANAR Mitundu pa bwalo la Dedza loweruka.
Timuyi inakwanitsa kupeza mapoints asanu ndi awiri pa masewero awo oyamba koma yagonja ndi Chitipa United, Karonga United ndiponso apa Mitundu kuti ataye mapoints ochuluka.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Emmanuel Zoya, wati timu yake yavomereza kugonja kamba koti Mitundu inali bwino paliponse.
"Zikutivutadi koma tikungoyenera tibwerere tikaunikire kuti pakutivuta ndi pati koma ndikutsimikiza kuti tibwereranso mwa mphamvu," anatero Zoya.
Iye anatinso kuvulala kwa China Chirwa komanso wotchinga pagolo Rahaman John kunawasokonezanso mmasewerowa kamba koti sanakonzekere kusewera opanda akatswiriwa.
Timu ya Civil tsopano yatsika kufika pa 10 pomwe ili ndi mapoints okwana asanu ndi awiri pa masewero asanu ndi imodzi.
0991769328
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores