"KOMA KWATHU NDE TIKUCHAPANI MUKABWERA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United wati anthu ayiwale kuti timu yake ituluka mu ligi poti ili ndi masewero asanu ndi atatu apakhomo komwe matimu onse akachokako akulira.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-2 ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets lamulungu pa bwalo la Kamuzu ndipo wati timu yake ili ndi mpata waukulu wokhalabe mu ligi.
"Tsogolo lilipo lowala kwambiri ndipo chaka cha mawa tisewera mu top 8 mudzandifunse mudzandikhulupilira, ndili ndi masewero 8 pakwathu nde pamene paja palibe angandisunthe ndi tchetchatchetcha basi, tizivutika tikayenda chonchi koma kwathu palibe." Anatero Nyambose.
Timuyi ili pa nambala 14 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 17 pa masewero 21 omwe yasewera chaka chino.
Chitipa yapambana kanayi, kufanana mphamvu kasanu ndi kugonja kakhumi ndi kawiri (12) ndipo yagoletsa zigoli 22 ndi kumwetsetsa 34.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr 📷: MMH photography
Tumizilani ku 0897788997
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores