KAONGA WAMWETSANSO KU ZAMBIA
Katswiri wa timu ya Flames, Chawanangwa Kaonga, wagoletsa chigoli chake chachiwiri mu zokonzekera za ligi ndi timu yake ya ZANACO pomwe dzulo anachokera panja ndikugoletsa kuti timu yake iphe Green Eagles 2-0.
Kaonga anamwetsa mpira umene anapatsilidwa pa kona ndipo sanayimitse koma nkuwuswera mu ukonde kuti ZANACO izitsogola 1-0 pa mphindi 62, nzake wina asanabwere mphindi khumi zotsatirazo.
Ichi chinali chigoli chake chachiwiri mu mpikisano wa matimu anayi omwe timuyi yatsiliza pa nambala yachitatu pambuyo pa akatswiri, Red Arrows ndi Zesco United ndipo Red Eagles yatsiliza pansi penipeni.
Kaonga anasankhidwa kukhala osewera wapamwamba mu mpikisano wa COSAFA Cup pomwe anathandiza timu ya Flames kuthera pa nambala yachinayi.
Zilibwino
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores