🚨 Messi vs Yamal Sakumana
Masewera a Finalissima amene amayeneleka kuchitika pakati pa Argentina national football team ndi Spain national football team alepheleka.
Masewerawa anali pakati pa opambana a UEFA Euro 2024 (Spain) ndi opambana a Copa América 2024 (Argentina).
Masewerawo achotsedwa chifukwa cha ndale zomwe zomwe zikuchitika m'dera limene masewerawo anali kuti achitike.
Poyamba masewerawo anakonzedwa kuchitikira ku Qatar pa 27 March, koma mabungwe a mpira a mayiko awiriwa sanagwirizane pa stadium ina pambuyo pa misonkhano yomwe anachita kuti apeze yankho.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores