Iran yalengeza kuti sitenga nawo mbali ku 2026 FIFA World Cup yomwe ikubwera Chaka chino.
Nduna ya zamasewera ku Iran, Ahmad Donyamali, yanena kuti chifukwa cha mavuto a chitetezo komanso kusamvana pakati pa Iran ndi United States, dzikolo silingathe kutenga nawo mbali pa mpikisanowu.
Iye anafotokoza kuti nkhondo ndi mikangano yomwe yachitika m'miyezi yapitayi yapha anthu masauzande ambiri, motero palibe zinthu zoyenera kuti Iran itenge nawo mbali pa World Cup.
Mpikisano wa 2026 FIFA World Cup omwe ukuyamba pa 11 June uchitikira m'mayiko atatu: United States of America,Canada Ndi Mexico.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores