''Timafunitsitsa kuti tipambane'' - Kajawa
Mphunzitsi watimu ya Mighty Tigers, Trevor Kajawa, wati ngati timu yake inakwanitsa kuteteza masewero onse koma akupereka ndi osewera mmodzi ndekuti yasewera bwino koma amafunitsitsa kupeza chipambano ma masewero awo ndi FCB Nyasa Big Bullets.
Iye amayankhula atatha kufanana mphamvu ndi Bullets pa bwalo la Mpira ku Chiwembe ndipo wati kusewera kwawo kwawalimbitsa mtima kuti atha kuchita bwino mmasewero awo omwe atsala.
''Sitingasangaliretu koma tikuyenera kuchilimika kuti tichite bwino mu masewero omwe tatsala nawo tichite bwino, point iyiyi kuti ndi yofunikira kwambiri chifukwa timafunsa kupambana,'' anatero Kajawa.
Iye wati ndi zotheka kuti timu yake kupulumuka mu ligi koma ndekuti ifunikira kupambana ma masewero omwe atsala nawo.
Tigers ikadali pa nambala 15 ndi mapoints 27 pa masewero 28 omwe asewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores