MATIPAPASI WATSANZIKA KU NYERERE
Katswiri wosewera pakati mu timu ya Mighty Wanderers, Balikinho Mwakanyongo, watsanzika kutimuyi pomwe tsopano wachokapo patatha zaka zitatu.
Katswiriyu walemba uthenga wotsanzika ndi kuthokoza Timuyi pokhala naye mu zakazi.
Mwakanyongo anachokera kutimu ya Karonga United ndipo anakhazikika kwambiri koma atabwererakonso nthawi yomwe anadzathawako sanapezenso mpata osewerasewera.
Oseweranso ena omwe achoka kutimuyi ndi Vincent Nyangulu, William Thole komanso Mischeck Botomani patsogolo pa ligi ya 2025.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores