Anthu akale munkaonera mpira weniweni
Ana amma 2000 tadyetserako maso. Ayi ndithu kale anthu mumaonera mipira yokoma ndithu ndipo chithunzithunzi chimachita kuoneka pa madhala omwe amamenya loweruka lapitali.
Masewero anayamba ndi timu ya osewera a Silver Strikers akale akukumana ndi Dynamos yaku Zimbabwe ndipotu anali masewero abwino kwambiri.
Zimachita kuonetsa kuti anyamata aluso anali aluso lochuluka zedi. Munamvapo za Peter Pindani inu? Loweruka nde watchaya mpiradi. Ndipo goloboyi wa timuyi Bright Nyasulu eh kugwira mwaluso ndipo mapenate awiri kumatiratu osalavula.
Nde kunabwera Derby ayi ndithu. Derby osadzayichepsa, miyala inaonekatu kamba kokwiya ndi oyimbira wothandizira yemwe anakweza mbendera kuti wina analowa malo osayenera komabe sizinali tero.
Komatu anyamata amaswa mpira. Kuona George Sangala, Valence Kamzere, Moses Chabvula, Victor Nyirenda, Lawrence Tikotiko Majawa ndi ena ku Wanderers, ayi ndithu mumanjoya.
Nde tinakumbutsira achina Gilbert Chirwa, Heston Munthali, Henry Kabichi, Yamikani Fodya, John Lanjesi, Sankhani Nyirenda ndi ena ku Bullets kumati komatu anyamata mmmh.
Fischer Kondowe inu mmene amadudukira, Robert Ng'ambi tinjomba, Francis Mlimbika kukokera patali, Peter Wadabwa mbambande haaa! anthuni mumanjoya.
Nkumadzifunsa kuti awa ngati akudoda chotere nde kalelo anthuwa amatani inu.
"Osewera ambiri akale anali ndi mphatso yakumvetsetsa choyenera kuchita nawo mpira kuposa ambiri apano ndipo kale kunali mpira wokoma." Anatero Kevin Moyo pakucheza nane.
Taonera mpira wa pansi, kupondana poti ndi mpira koma luso linalipo ndipo zigoli zokongola kwambiri. Kale timu simangochoka kumpoto kudzatuta 10-0 nkumapita ndithu koma umayaka ndithu.
Ngakhale tinakondwa ndithu komabe tinachoka ndi mafunso kuti mukuti ma Legends kapena ma former players? Ili mwana wa 2000 anakanika kuyankha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores