Bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo mdziko muno la FAM lati Hassan Kajoke akhozabe kumatumikira timu ya FCB Nyasa Big Bullets.
FAM yatero kufikira komiti yowona za osewera (Players' Status Committe) itamaliza kuwunikira nkhani yokhudzana ndi mgwirizano womwe a Silver Strikers akuti adasaina wosewerayu.
Mkulu wowona za malonda a osewera ndi kupereka ziphaso ku FAM, a Casper Jangale, ati mundondomeko yawo zikusonyeza kuti Kajoke ndi wosewera wa Bullets.
A Jangale atsimikiza kuti komitiyi yalandira umboni umene inafunsa timu ya Silver Strikers kuti itulutse wowonetsa kuti Kajoke anasayina mgwirizano wa zaka zitatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores