Goloboyi wakale wa timu ya dziko lino ya Flames, Boniface Maganga wamwalira.
A Maganga atisiya lero pa chipatala cha Queen Elizabeth mu mzinda wa Blantyre komwe amalandira thandizo la chipatala.
Maganga anali goloboyi wa Flames kuyambira chaka 1969 ndipo anali m'modzi mwa akatswiri omwe anathandiza Malawi kutenga chikho cha East and Central Africa Senior Challenge Cup mu 1978 ndi 1979.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores