Man dia
Kamuzu balakis
FAM YAYANKHAPO PA NKHANI YA SILVER NDI PANTHERS
Bungwe la Football Association of Malawi layankhulapo pa dandaulo lomwe timu ya Silver Strikers linapereka ku bungweli loti timu ya Panthers linagwiritsa ntchito osewera omwe anasewera kale mu mpikisanowu.
Bungweli ladzudzula timu ya Silver kuti silinatsate ndondomeko yoyenera podandaula pa nkhaniyi molingana ndi malamulo oyendetsera mpikisanowu pa gawo 14.1.1 komanso 14.1.2.
Ilo latinso bungweli likhazikitsa komiti yatsopano kuti ifufuze za nkhaniyi kutanthauza kuti kufikira panopa nkhaniyi siyinathe tsopano.
Timu ya Silver inadandaula pa nkhaniyi atagonja 4-3 pa mapenate ndi timu ya Panthers ndipo inati osewera awiri, Taniel Mhango komanso Aggrey Msowoya sanali ololedwa kusewera masewerowa poti anasewerakonso ku matimu enanso.