SONGWE IKUYANG'ANA ZOBWERERA MU LIGI YAIKULU
Mphunzitsi watimu ya Songwe Border United Elias Chirambo wati ndi wokondwa ndi momwe timu yake ikuchitira ndipo zikulingana ndi khumbo la anthu aku Karonga kuti timuyi ilowe mu ligi yaikulu.
Iye amayankhula atapambana 2-0 ndi Chilobwe United kuti apitilire kutsogolabe mu ligi ya NBS Bank National Division mu sabata yachisanu ndi chiwiri.
Chirambo yati boma la Karonga limakhala ndi matimu awiri mu ligi yaikulu ndipo kuchoka kwa Baka City yomwe inagulidwa ndi Masters FC kukuwakankha kuti alimbikire kuti alowenso mu ligi yaikuluyi.
"Ndi khumbo lathu komanso anthu aku Karonga kuti tibwerere mu ligi yaikulu chifukwa kuno nde kulikulu la mpira kumpoto kuno nde timakhala ndi matimu awiri mu ligi yaikulu," anatero Chirambo.
Iye wathokoza anthu amu bomali komanso akuluakulu a timuyi kamba kowathandiza mu njira zambiri zomwe zikuwathandizanso kuti azichita bwino.
Songwe ili pa nambala yoyamba ndi mapoints 16 itapambana kasanu, kufanana mphamvu k
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores