FAM, SULOM amvana chimodzi
Mabungwe a Football Association of Malawi komanso Super League of Malawi onse amvana kuti masewero otsegulira ligi ya FDH Premiership achitikebe pa bwalo la Kamuzu ngakhale analipezera zolakwika.
Mtsogoleri wa bungwe la SULOM, Brigadier Gilbert Mittawa, watsimikiza za nkhaniyi pomwe wati apempha ku FAM kuvomera bwaloli kuchititsa mwambowu kamba koti ndi bwalo lalikulu.
Iye wati zolakwika zomwe zinali pa bwaloli zina zakonzedwa ndipo zina zidzakonzedwa masewerowa akhadzatha kupereka mpata kuti adzayenderenso bwaloli.
Matimu a Mighty Wanderers komanso Karonga United ndi omwe adzakumane pa masewero enieni otsegulilira ligi ya FDH Premiership ya chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores