NKHANI
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yamvana ndi timu ya Civil Service United kuti atenge katswiri womwetsa zigoli, Dastan Banda.
Katswiri wa zaka 25 yu wakhala osewera ofunikira kwambiri ku timu ya Civil pomwe anamwetsa zigoli 9 mu ligi yaikulu ya m'dziko muno.
Timuyi yatenga Banda ngati mlowammalo wa Babatunde Adepoju yemwe anapita ku timu yake ya Venda Football Club ku South Africa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores