Dziko la Morocco latsimikiza kuti lasiyana ndi mphunzitsi watimu ya dziko lawolo, Walid Regragui, pompopompo mopanda kulingalirq kawiri katatu.
Mphunzitsiyu waphunzitsako masewero 49 ku timuyi ndipo anapambana 36, kufanana mphamvu kasanu ndi katatu (8) ndi kugonja kasanu (5) kenikenitu.
Pa masewero 49 amenewa, Morocco inagoletsa zigoli 101 ndipo inagoletsetsa 21 zokha basi. Mu nthawi yake, timuyi yafika mu ndime ya matimu anayi a World Cup komanso ndime yotsiriza ya AFCON.
Ndipo Mohamed Ouahbi uja anatsogolera timu ya dzikolo yosapyola zaka 20 kutenga chikho cha FIFA World Cup, ndi yemwe wakonzeka kuti atenge ntchitoyi.!
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores