"Masewero ake akakhala ovuta" - Ngwira
Mphunzitsi watimu ya Goshen City Dedza Dynamos wati akuyembekezera kuti masewero awo ndi Blue Eagles akhala ovuta kwambiri koma akonzeka kuti achite bwino mmasewerowa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo amu chikho cha Castel mu ndime ya matimu anayi pomwe akumane pa bwalo la Kamuzu loweruka.
Iye wati anyamata akonzekera bwino ndipo palibe choopsa chilichonse chomwe chikuwafooketsa pa masewerowa.
"Mabwalo onse omwe ali mdziko muno ambiri tinasewerapo nde si achilendo zomwe zikusonyeza kuti ndife okonzeka kusewera paliponse," iye anatero.
Ngwira wamemanso ochemerera atimuyi kufika pa bwaloli kuti adzawapatse mphamvu ndi cholinga choti akafike mu ndime yotsiriza.
Dynamos yakumana kale ndi Blue Eagles kawiri mu ligi ndipo anapambana kamodzi ndi kufananitsa mphamvu enawo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores