"Sitinapange chiganizo cha chitsogolo chathu" - Sobhuza
Kampani ya TNM yati ikhala pansi ndi kuunikira chitsogolo chawo Komanso mapempho onse omwe abwera ku nkhani ya kuthandiza nkhani za masewero pakuti zinthu zinachitika modzidzimuka kwambiri pomwe anachalira kuthandizabe Supa ligi.
Mkulu woona za malonda ku kampaniyi a Sobhuza Ngwenya anayankhula izi pa mwambo wopereka mphoto kwa omwe anachita bwino mu 2025 ndipo iwo anati anasunga lonjezo posafuna kuchoka mwa chipongwe.
Iwo ati mapempho omwe boma, Football Association of Malawi ndi anthu ena opitilizabe kuthandiza ku mpira awamva koma sangapange chiganizo asanaunikire chitsogolo chawo.
"Tinali okonzeka kuthandizanso mu chaka cha 2026 koma zinthu zake zinachitika mwa changu nde panopa kuti ndifotokozere chitsogolo chathu ndekuti ndidya mfulumira, tikakhale psnsi kaye tidzanena," anatero Ngwenya.
Kampaniyi yakhala ikuthandiza ligiyi kwa zaka 18 kuchokera mu 2006 koma pano SULOM yapeza FDH Bank ngati wowathandiza watsopano.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores