SULOM ipitilira kugwirabe ndi TNM
Bungwe la Super League of Malawi lati pali zinthu zochuluka zimene sizingachokeretu kuchokera ku kampani ya TNM zomwe zichititsebe kuti mbali ziwirizi zizigwirirabe ntchito limodzi.
Mtsogoleri wa bungweli Brigadier Gilbert Mitawa ati palibe chilichonse chomwe chidzafufute mbiri ya TNM pakuti yathandiza kutukula mpira wa mdziko muno.
Iye wati TNM inafika mu nthawi yomwe mpira unali wotsika kwambiri koma tsopano wakwera kwambiri kamba ka thandizo lawo mu zaka 18 zadutsazi.
"Ndi oti ali ndi zambiri chitsanzo kadi la mpata lomwe linali ndi mphamvu kugula tikiti pa makina a intaneti ndekuti zikhala zikufunikirabe nde tikhala nawo pansi kuunguza ndi iwo momwe tingapitilizire kugwiritsa nawo zinthuzi," anatero Mitawa.
Bungweli padakali pano linapeza FDH Bank ngati wothandiza ligiyi kwa zaka zisanu zikubwera kutsogoloko poonjezera kawiri ndalama zomwe TNM inkayika.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores