Khungwa, Salima, Babatunde ndi Wanderers alandira mphoto lero
Kampani ya lamya za mmanja ya TNM ikuyembekezeka kupereka mphoto kwa Mighty Wanderers komanso osewera monga Dalitso Khungwa, Chikumbutso Salima, Babatunde Adepoju ndi ena kamba kochita bwino mu chaka cha 2025.
Kampaniyi yakonza mwambo wopereka mphotozi madzulo a lero pa 05 February 2026 ku hotela ya Mount Soche ku Blantyre.
Iwo ati mwambowu ndi mbali imodzi yokondwerera zaka 19 zomwe akhala akuthandiza ligi yaikulu ya dziko lino kuchokera mu 2006.
Pa mwambowu, katswiri wosewera bwibo kuposa onse, omwetsa zigoli zochuluka, wotchinga kumbuyo wabwino, wapakati, mphunzitsi wabwino, oyimbira ndi akatswiri a ligi akapatsidwa mphoto.
Ndipo atolankhaninso nawo akapatsidwa ulemu pa ntchito yomwe agwira mu chakachi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores