''A GILBERT CHIRWA NDEKUTI AKUKAONA ABALE AWO'' - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati uthenga womwe wachiwiri kwa mphunzitsi wa FCB Nyasa Big Bullets, Gilbert Chirwa, amanena kuti akupita ku Mzuzu komweko ndekuti unali woti akukaona abale awo osati kuchalira Moyale.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anagonja 3-0 ndi timu ya Civil Service United lamulungu ndipo anati iwo uthenga umenewo sukuwakhudza.
''Paja ine ndi waku Mzuzu nde a Gilbert Chirwanso ndi akonko nde mwina akukaona abale awo. Ngati anakuuzani choncho ayi ndithu ife sizikutikhudza mwina amanena ndi akwawo,'' anatero Mwansa.
Koma iye anati kugonja kwawo ndi Civil kwawapatsa phunziro lalikulu loti alimbikire mu masewero omwe atsala nawo mu ligiyi ndi kuti asatuluke.
Moyale ikumana ndi timu ya Bullets lachitatu pa bwalo la Mzuzu pa masewero omwe matimu onse akufunikira mapoints atatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores