''HAMMERS IKHALA YOYAMBA KUSWA WANDERERS'' - NYEMERA
Wachiwiri kwa mphunzitsi wa timu ya Mzuzu City Hammers, Lazarus Deco Nyemera, wamema ochemerera atimuyi kuti afike pa bwalo la Mzuzu kudzachitira umboni iwo akugonjetsa Mighty Wanderers lachitatu masana.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe matimu onse akufunikira kupeza chipambano kamba koti Hammers ikufuna kupulumuka mu ligi pomwe Wanderers ikufuna kutenga chikho.
Iye wati osewera ake akonzeks ndipo achite bwino pa masewerowa.
''Molalo ili pa mwamba malingana ndi masewero atatu a m'mbuyomu omwe tasewera ndipo anyamata akuoneka kuti alibwino kwambiri moti tikachita bwino,'' iye anatero.
Nyemera watinso timuyi ilibe vuto la kuvulala kwa osewera mu timuyi ndipo onse ndi okonzeka kukagwira ntchito.
Chipambano cha Hammers chitha kuwafikitsa pa ma points 27 panambala 14 kuti ayandikire kutuluka mu chigwa cha matimu otuluka mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores