WANDERERS ILI NDI MWAYI WOSANKHA KAPENA KUTHAWA BULLETS
Timu ya Mighty Wanderers ichita kusankha yokha kuti isewere ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets posachedwapa kapena ayi pomwe matimuwa akhonza kukumana mu ndime ya matimu anayi a chikho cha FDH Bank.
Izi zikudza kutsatira kuti Bullets yadutsa mu ndime ya matimu asanu ndi atatu kusonyeza kuti akungodikira kuti akumane ndi wopambana pakati pa Manoma ndi Creck Sporting Club.
Bullets ikuyang'ana kufikanso ndime ina yotsiriza mu chikhochi pomwe Wanderers sinapambaneko chikhochi ndipo yaika mtaji woti chaka chino chokha atenge chikhochi.
Chisankho chikhale ndi Wanderers kuti ikumane ndi Bullets kapena kuyizemba kuti Creck Sporting Club ipite kokumana ndi Bullets ndipo zidziwika mphindi 90 zikatha pa bwalo la Champions.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores