"Tigwiritsa ntchito mwayi wosewerera pakhomo" - Chidati
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Wilson Chidati, wati timu yake yakonzeka kuyamba ligi ya 2025 ndipo igwiritse ntchito mwayi wosewerera pakhomo kuti achite bwino mu masewero oyamba.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Karonga United omwe aliko pa bwalo la Nankhaka mu mzinda wa Lilongwe lamulungu masana.
Iye wati timu yake yonse ilipo ndipo anyamata akonzekera bwino ndipo kusintha bwalo kuchoka ku Civo kupita pa Nankhaka si vuto kwenikweni.
"Molalo ndi yaikulu kwambiri mu timuyi ndipo anyamata akonzeka bwino kwabasi akungodikira masewerowo nde Tigwiritsa ntchito mwayi wosewerera pakhomo." Iye anatero.
Timuyi ikuyamba masewerowa ili ndi mulingo omwe anapatsidwa kuti adzamalize mu matimu atatu oyambilira mu ligi komanso kupambanako chikho chimodzi.
Pa 0981658760
Tumizani Ku 0991509953
Ku 0897788997
Nonse takutimizirani ndalama zanu. Zikomo 👏👏
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores