Haiya: Tabitha, Temwa ndi akunja onse abwera
Mtsogoleri wa bungwe loyendetsa mpira mdziko muno la Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, wati timu ya Scorchers ikhale ndi osewera ake onse omwe imadalira.
Iye amayankhula lachitatu pa mwambo omwe bungweli limayankhula pa zinthu zosiyanasiyana ku Chiwembe ndipo amatsimikiza kuti ulendo waku Zambia ulipo.
Iye wati Zambia ikhale ikutenganso timu yawo yonse yomwe amadalira chomwechonso Malawi itero.
"Achina Tabitha, Temwa ndi ena onse timawadalira kunja tikuwadziwa akhale akubwera pa masewero amenewa nde ena azifika mma 15 February ena pa 16." Anatero Haiya.
Iye anatinso komiti yaikulu ya FAM inakambirana kuti Scorchers izisewera mmipikisano yonse yomwe azikhudzidwa poti amangosewera COSAFA yokha.
Timuyi ikasewera masewero apaubale awiri ndi Zambia ngati njira imodzi yosafuna kungokhala poti timu yomwe ankafuna kukumana nayo mu masewero opitira ku WAFCON, Congo, inati siseweranso.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores