"EKHAYA IDZAKHALA NDI BWALO LAKE" - MPINGANJIRA
Mtsogoleri wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Dr Thomson Mpinganjira, watsimikiza kuti palibe mpata woti akhonza kusiya kuthandiza timuyi ngati Ekhaya FC italowe mu ligi poti Kampani imatha kuthandiza matimu angapo.
Iye amayankhula atafunsidwa ngati kulowa kwa Ekhaya mu Supa ligi kumuchotse ku Wanderers poti Ekhaya ndi imodzi mwa ma Kampani awo komanso imathandiza Wanderers.
Iye anati, "Ine ndinapita ku Wanderers mwa ndekha ngati munthu poti Wanderers ndi timu yomwe ndakhala ndikusapota. Ekhaya kunali kungogulitsa dzinali koma mu ma Kampani athu muli magulu atatu, Ekhaya, Renaissance ndi ineyo nde ndi mphekesera chabe."
Iye anatinso kunja kwa dziko lino matimu ambiri amathandizidwa ndi Kampani ya Fly Emirates ndipo sizachilendo kuti Ekhaya ithandize Ekhaya FC ndi Wanderers.
Iye wati Ekhaya mtsogolomu idzakhala ndi bwalo lake lomwe timuyi pamodzi ndi Mighty Mukuru Wanderers adzagwiritsa ntchito ngati bwalo lawo lapakhomo ndipo amafun
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores