"TIMU IDZAKHALAPO IWO AKAPITA" - MPINGANJIRA
Mtsogoleri wa Mighty Mukuru Wanderers, Dr Thomson Mpinganjira, wanenetsa kuti osewera atatu omwe amalimbikitsa mchitidwe wolakwika kutimuyi achotsedwa ndithu mosawanyengerera.
Iye amayankhula utatha mwambo wopereka mphoto kwa osewera omwe achita bwino mu chaka cha 2024 ndipo wati osewerawa anachita khalidwe lonyasa.
Iye wati sangadandaule za kuchoka kwa timuyi poti iwo ndi osewera chabe ndipo akachoka timu siyitha.
"Amenewatu akuchoka ndithu chifukwa anachita zinthu zonyasa kwambiri nde sitingamasekerere zoterezi. Achoka timu ikhalapobe." Anatero Mpinganjira.
Osewera atatuwa sanatchulidwe mayina ndi mtsogoleriyu ndipo sanapereke mpata wowakhazika pansi ndi kuwachenjeza.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores