"NGATI SI BOB TITENGA KUNJA" - MPINGANJIRA
Mtsogoleri wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers wati zokhudza mphunzitsi watimuyi mu chaka cha 2025 sanakambirane koma zichitika posachedwapa.
Iye amayankhula izi usiku wa lachiwiri pa mwambo wopereka mphoto kwa osewera omwe achita bwino kutimuyi ndipo wati timu padakali Pano ikadali mmanja mwa Bob Mpinganjira.
Iye wati timu yake sikutenganso mphunzitsi wamdziko momwe muno ndipo ngati samusiyirabe Bob Mpinganjira ndekuti akatenga mphunzitsi wakunja.
"Timu ili mmanja mwa Bob Kaye apapa koma tikakambirana ndekuti tikuuzani kuti ndi ndani koma sitingatenge wamdziko momwe muno ayi, ngati sakhala Bob ndekuti titenga kunja tione zina." Anatero Mpinganjira.
Chaka chatha, timuyi inaona aphunzitsi awo awiri, Nsanzurwimo Ramadan ndi Meke Mwase akuchoka kutimuyi osatsanzika koma Bob Mpinganjira ndi yemwe anayitenga ndi kupambanakonso chikho.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores