"SI MPHAMVU YANGA KOMA ZA YAHWEH" - KALIATI
Katswiri wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Isaac Kaliati, sanazitamandire iye mwini koma watchula Mulungu mu zoyankhula zake zonse pounikira momwe wachitira mu chaka cha 2024.
Kaliati amayankhula utatha mwambo wopereka mphoto kwa osewera omwe achita bwino ku timuyi ndipo iye anasesa mphoto zinayi ku mwambowu kamba chochita bwino mu chakachi.
Iye anasankhidwa ngati wosewera wapamwamba pakati pa timuyi, osewera yemwe wazitolera kwambiri, osewera yemwe wamwetsa zigoli zambiri komanso osewera woposa aliyense kutimuyi.
Iye anati, "Ndikuthokoza Mulungu kamba ka Chisomo chake sikuti ndi mphamvu zanga ayi koma ndi mphamvu yake."
Kaliati anakwanitsa kugoletsa zigoli zokwana 22 ndi kuthandizira zigoli zokwana 14 pa masewero onse omwe wasewera mu mipikisano yonse kutimuyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores