NYASULU WATHOKOZA PASUWA POMUKHULUPILIRA
Katswiri wotseka kumbuyo kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Nickson Nyasulu, wathokoza mphunzitsi watimu yake, Kalisto Pasuwa, kamba komukhulupilira mu chakachi zomwe zamuthandiza kusewera mmasewero ochuluka kwambiri.
Iye amayankhula atatha kupatsidwa mphoto ya osewera yemwe wasewera bwino kumbuyo kwa timuyi komanso kutimu yonse mu chaka cha 2024 pa mwambo omwe timuyi inakonza usiku wa lolemba.
Iye wati ngakhale ligi ya chakachi inali yovuta, Pasuwa anamukhulupilira mu masewero ochuluka.
"Inali season yovuta kwambiri komabe mphunzitsi anandikhulupilira kuti ndisewere mmasewero ochuluka kwambiri ndikuwathokoza kwambiri." Anatero Nyasulu.
Katswiriyu anakwanitsa kugoletsa chigoli chimodzi ndi kuthandizira chigolinso chimodzi pa masewero onse omwe wasewera kutimuyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores